MALILIME
MALILIME
  • Changamire M'zizi
  • 승인 2022.11.01 18:15
  • 댓글 0
  • 조회수 551
이 기사를 공유합니다

. Changamire M’zizi (Kantini Samson) is a Zambian poet, a development educationalist, and a cultural historian. He is interested in the aims, the strategies, and the content of the socialization and transformative processes that they ought to have in place to create, promote and raise the critical consciousness of wholeness in low-resourced environments in order to bridge the divide between the worlds of rich and poor, and the theory and practice for sustainable societies. He holds a Ph.D. in Education from Seoul National University, an MEd in Education and Development from The University of Zambia (UNZA), an MA in Literature, and a BA in Education (BAEd) also from UNZA. He has received a Certificate in Diplomatic Practice, Protocol, and Public Relations from the Zambia Institute of Diplomacy and International Studies (ZIDIS). Currently, He is Senior Programme Officer for Culture, Communication and Information at the Zambia National Commission for the United Nations Educational, Scientific and Cultural Organisation (UNESCO)

냔자어/체와어(Nyanja/Chewa) : 체와어(Chewa)는 말라위의 공용어이다. 니제르콩고어족에 속하며 냔자어(Nanja)로도 알려져 있다. 시인은 모어(母語)인 냔자어(Nyanja)/체와어(Chewa)로 이야기의 내용, 그 속의 인물들, 그것이 지니는 문화적 가치 등의 이미지와 격언과 비유를 표현한다.

 

 

Titwe, titwe
Iyayi titwe dangaza
Akazi amfumu
Alowa msitolo
Namchila wa ng’ombe
Nandodo kumanja
Iyayi titwe dangaza

Ndinabadwa ndi lilime
Mukamwa mwanga lilicikhalire
Apo linati lilankhuleko
Mano anatulukira mukamwa mwanga
Kuti atangatile lilime langa
Pafupi-fupi ndi bongo-bongo yanga;
Pansi-pansi pa maso anga
Cifukwa lilime langa ndi masompenya anga,
Maganizidwe anga, cithethezo canga.

Inde, ndinabadwa ndi lilime
Liri pakati-kati kamakhutu anga
Pakuti lilime langa
Ndiko kumva kwanga konse
Lidziwathu zanga zonse
Zonse zakudya zopikidwa ndi agogo pamoto.
Koma sukulu, sukulu ladula lilime langa

Kuliyetsa ngati mbuli
Yosadziwa tushampeni
Koma cabe munkoyo ndi kachasu
Uyu ndithu ndi wenye.
Paja akulu amati: nguwo yobwereka siilimba m’thupi
Ili lilime lobwereka sukulu yasoka-soka mkamwa mwanga
Silidziwa Lumanda
Silidziwa Vinkubala
Kolowa ndi Chikanda
Masuku ndi Matondo

Ili lilime lobwereka
Silidziwa Ciyato
Silidziwa Nsolo
Cidunu Kabishabisha
Walyako Walya Ndimu
Vikuti naMukule

Ana azakula bwanji
Omwe ndi tsogolo lanu makholo
Abemba amati: ‘Imitikula empanga’
Koma zili kucitika mumpangamo
Imitikula ikakula, igulitsidwa Mukula
Kukula kwa m’masukulu
Kupanga ana azungu
Osayankula lilime la cimunthu
Cimunthu cathu akakamba kapena kulemba
Apanishidwa ndi aticha

 


댓글삭제
삭제한 댓글은 다시 복구할 수 없습니다.
그래도 삭제하시겠습니까?
댓글 0
댓글쓰기
계정을 선택하시면 로그인·계정인증을 통해
댓글을 남기실 수 있습니다.